Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:34 - Buku Lopatulika

34 Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Ndikukupemphani tsono mudye kanthu kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzataye ngakhale tsitsi limodzi la kumutu kwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:34
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.


komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.


Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.


komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.


Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.


Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu.


Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,


Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.


Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa