Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:12 - Buku Lopatulika

12 Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono mkaziyo adati, “Chonde, mulole kuti ine mdzakazi wanu ndilankhule mau ena kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumuyo idamuuza kuti, “Lankhulani, mai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kenaka mkaziyo anati, “Lolani kuti wantchito wanu ayankhule mawu kwa inu mbuye wanga mfumu.” Iye anayankha kuti, “Yankhula.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:


Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.


Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.


Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.


Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.


Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.


Anatinso, Ndili nanu mau. Nati iye, Tanena.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:


Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa