Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:21 - Buku Lopatulika

21 kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 kapena kumpanda ndi dzanja lake modana naye, mnzakeyo naafa, ndiye kuti amene adamenya mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ndi wopha munthu ameneyo. Mbale wa munthu wakufayo ndiye aphe wopha mnzakeyo akangokumana naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 kapena ngati, chifukwa cha udani, amenya mnzake ndi nkhonya, mnzakeyo ndi kufa, munthuyo ayenera kuphedwa. Iyeyo ndi wakupha. Wolipsira adzamuphe wakuphayo pamene akumana naye.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:21
7 Mawu Ofanana  

Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.


Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.


Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.


Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.


Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.


Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;


Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa