Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
2 Akorinto 1:4 - Buku Lopatulika wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. |
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.
Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.
Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.
Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.