Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 14:26 - Buku Lopatulika

26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 14:26
75 Mawu Ofanana  

Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.


Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.


Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.


Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;


Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,


Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.


ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.


Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.


Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.


Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,


Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.


Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.


Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.


Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.


Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.


Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.


Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m'ngalawa ku Kipro.


Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;


Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;


Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,


Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?


Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.


Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,


Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.


kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.


Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.


Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;


Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,


kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.


zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,


Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.


Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.


Pakuti pali atatu akuchita umboni,


Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera,


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa