Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
1 Samueli 20:1 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide adathaŵa ku Nayoti ku Rama, nabwera kwa Yonatani. Ndipo adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndidachita chiyani? Ndidalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndidaŵachimwira chiyani, kuti azifuna kundipha?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?” |
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.
Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti.
Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.
Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji?
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.
Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.
Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa.
Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani?