Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:3 - Buku Lopatulika

3 Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ine ndili pompano, ngati chilipo chimene ndidalakwa, munditsutsiretu tsopano pamaso pa Chauta ndi pamaso pa wodzozedwa wake. Kodi ndani ndidamulandapo ng'ombe? Ndani ndidamulandapo bulu? Ndani ndidamdyererapo? Kodi ndani amene ndidamuzunza? Kodi nkwa yani ndidalandirapo chiphuphu choti nkundidetsa m'maso? Tsimikizeni, ndipo ndikubwezerani zonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:3
29 Mawu Ofanana  

Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.


Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.


Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.


Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.


Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.


Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama.


Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.


pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;


kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.


Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.


Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.


Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.


Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Ndipo iwo anati, Simunatinyenge, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense.


Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeze kanthu m'dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni.


Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake.


Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.


Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa