Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 10:27 - Buku Lopatulika

Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma anthu ena achabechabe adati, “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipulumutsa ife?” Ndipo adayamba kumnyoza Sauloyo, osampatsa ndi mphatso zomwe. Koma iye adangokhala chete.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.

Onani mutuwo



1 Samueli 10:27
21 Mawu Ofanana  

Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.


Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndi mure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.


Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.


Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwapambana.


Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.


Koma ine, monga gonthi, sindimva; ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;


Koma iwo anakhala chete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.


Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;


Ndipo anthu anati kwa Samuele, Ndani iye amene anati, Kodi Saulo adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe.


Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso mu Israele.


Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.


Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.


Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.