Machitidwe a Atumwi 7:35 - Buku Lopatulika35 Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 “Moseyo ndi yemwe uja amene Aisraele aja adaamkana nkumanena kuti, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu?’ Yemweyo Mulungu adamtuma kuti akhale mkulu ndi momboli kudzera mwa mngelo uja amene adaamuwonekera pa chitsamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 “Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba. Onani mutuwo |