Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 20:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zidangochitika kuti kumeneko kunali munthu wina wachabechabe dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini. Iyeyo tsiku lina adaliza lipenga, nati, “Ife tilibe chathu mu ufumu wa Davide, tilibe choloŵa mwa mwana wa Yese! Inu Aisraele, aliyense apite kunyumba kwake!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti, “Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide, tilibe gawo mwa mwana wa Yese! Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 20:1
31 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.


Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.


Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.


Ndipo anatero Simei pakutukwana, Choka, choka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;


Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.


Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira ku Yerusalemu.


Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.


Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya, pakuti siigwiridwa ndi dzanja;


Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.


ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.


Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvere anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao.


Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?


Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;


Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.


Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto; momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.


Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sungathe kukhazikika.


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.


Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;


Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mzindawo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.


Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye.


Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.


Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.


Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.


Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuke nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa