Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo anthu a Israele anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tili ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; chifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo anthu a Israele anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tili ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; chifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Apo Aisraelewo adayankha Ayuda aja kuti, “Tili ndi zigawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo mwa ufumu wa Davide ife tili ndi zigawo zambiri kupambana inu. Nanga chifukwa chiyani tsono mukutinyoza? Kodi ife sindife amene tidayamba kulankhula zoti mfumu yathu ibwerenso?” Koma anthu a ku Yuda adalankhula mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?” Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:43
23 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.


Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.


Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.


Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.


Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.


Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.


Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.


Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta, kulanda mzinda wolimba nkosavuta; makangano akunga mipiringidzo ya linga.


Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.


Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.


kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,


Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.


musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;


Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.


Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.


Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa