Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:21 - Buku Lopatulika

21 Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula, mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:21
7 Mawu Ofanana  

Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?


Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.


Usanamizire kapolo kwa mbuyake, kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.


pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.


amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.


Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa