2 Samueli 8:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Kenaka Davide adagonjetsa Amowabu. Adalamula onsewo kuti agone pansi m'mizere itatu pa gulu lililonse. Pagulu lililonse anali kupha anthu amene anali pa mizere iŵiri yoyamba, kusiyapo a mzere wachitatu. Choncho Amowabu adasanduka akapolo a Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho. Onani mutuwo |