1 Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma. 2 Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao. 3 Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani? 4 Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m'michera ya munda. 5 Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera. 6 Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake. 7 Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi. 8 Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni. 9 Israele, wachimwa kuyambira masiku a Gibea; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a chosalungama siinawapeze ku Gibea. 10 Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri. 11 Ndipo Efuremu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lake lokoma; ndidzamsenzetsa Efuremu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya chibuluma chake. 12 Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo. 13 Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu. 14 Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake. 15 Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi