Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 10:13 - Buku Lopatulika

13 Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mudabzala zolakwa, ndipo mudakolola chilango chake. Mwadya zotsatira zake za mabodza. Chifukwa choti mwadalira magaleta anu, ndi kuchuluka kwa anthu anu a nkhondo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma inu munadzala zolakwa, mwakolola zoyipa; mwadya chipatso cha chinyengo. Chifukwa mumadalira mphamvu zanu ndiponso ankhondo anu ochulukawo,

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 10:13
19 Mawu Ofanana  

Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo.


Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.


Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.


Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.


momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.


Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.


Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka.


Wofesa zosalungama adzakolola tsoka; ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.


Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.


Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.


Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.


Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa