Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -



60 Mau a M'Baibulo Odala Dziko la Israeli

60 Mau a M'Baibulo Odala Dziko la Israeli

Ndikufuna ndikuuzani nkhani yofunika kwambiri yokhudza Israyeli. Mulungu, m’mawu ake oyera, anasankha Israyeli pakati pa mitundu yonse ya anthu kuti adzionetse yekha ulemerero wake. Izi zikutiphunzitsa ife tonse zambiri.

Mulungu ankafuna kuti Israyeli ikhale chitsanzo kwa mitundu yonse, ndipo kudzera mwa iwo, “mabanja onse a dziko lapansi” adadalitsidwe. Tangoganizani kukoma mtima kwa Mulungu! Ngakhale pamene anthu a ku Israyeli anapereka Khristu kuti akapachikidwe, Mulungu adasunga otsalira. Zimenezi zimanditsitsimula kwambiri.

Chifundo cha Mulungu ndi chachikulu kwambiri! Tiyeni tipempherere otsalira a ku Israyeli ndi kuwadalitsa anthu onse okhala m’dzikomo. Baibulo limatiuza kuti wodalitsa Israyeli adzadalitsidwanso. Ndikuganiza kuti ndi lonjezo lamphamvu kwambiri.

Ndipo pamene tikudalitsa Israyeli, tisaiwale kudalitsa mitundu yonse ya dziko lapansi. Mulungu amatikonda tonse.




Genesis 12:2

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:23

Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 19:24

Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati padziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:13

ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 9:22

Ndipo Aroni anakweza dzanja lake kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 26:3

khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 48:20

Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 12:3

ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:9

Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 49:25

Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:16

popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 122:6

Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:1-2

Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu. Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye. Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa. Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo? Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye? Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha? Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono. Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza. Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake. Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani? Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:1

Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 39:5

Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 8:13

Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:11

Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:1-2

Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha. Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:15

Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:18-19

Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo. Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:5

Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:7

Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:27

Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 2:8

Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:8

Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 137:5-6

Ndikakuiwalani, Yerusalemu, dzanja lamanja langa liiwale luso lake. Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 30:30

Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:10

Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:12-13

Yehova watikumbukira; adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israele; adzadalitsa nyumba ya Aroni. Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 3:8

Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 22:18

m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:14

mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:7

Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:4

ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:22

Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako aamuna pa chifuwa chao, ndi ana ako aakazi adzatengedwa pa mapewa ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 132:13-14

pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti, Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:1-2

Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:21-22

Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao; ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 62:6-7

Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete, ndipo musamlole akhale chete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 27:29

Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:4

Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:5

Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:24-26

Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu. Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse. Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:2-3

Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako. Pakuti iwe udzafalikira ponse padzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 87:1-3

Maziko ake ali m'mapiri oyera. Yehova akonda zipata za Ziyoni koposa zokhalamo zonse za Yakobo. Mzinda wa Mulungu, inu, akunenerani zakukulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 12:10

Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:26-27

Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso. Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:14-15

Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu. Odalitsika inu a kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:22-23

Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako aamuna pa chifuwa chao, ndi ana ako aakazi adzatengedwa pa mapewa ao. Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:10

Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:1-2

Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake. Gulu lanu linakhala m'dziko muja. Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu. Ambuye anapatsa mau, akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu. Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha. Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira. Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala mu Zalimoni. Phiri la Basani ndilo phiri la Mulungu; Phiri la Basani ndilo phiri la mitumitu. Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha. Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika. Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao. Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu. Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:8

Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 1:11

Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:2-3

Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze; kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu. Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti? Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:26

ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:19-20

Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu; nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:4

Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu; akulemekezani chilemekezere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:34-35

Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu; ukulu wake uli pa Israele, ndi mphamvu yake m'mitambo. Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyamba ndi chitsiriziro. Ambuye, mibadwo yonse ya anthu anu idalitsidwe, pakati pa mikangano ndi nkhondo mukhale inu mukulimbana nkhondo za mtundu wanu wokondedwa, Israyeli adalitsidwe ndi zonse zomwe akukhala, kulowa ndi kutuluka kwake kudalitsidwe, chisomo chanu, chiyanjo chanu ndi chifundo chanu zimuzungulire nthawi zonse. Mtendere wanu wopambana chidziwitso chonse ukhale pamitima yawo, ndikupemphaninso kuti azindikire m'miyoyo yawo pangano latsopano la chipulumutso, lomwe munakhazikitsa kale pamtanda kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu. Ambuye, mawu anu amati: “Ndidalitsa amene akudalitsani, ndipo amene akukutsembani ndidzawatsutsa; ndipo mwa inu mitundu yonse ya dziko lapansi idalitsidwa.” Mulungu wanga, sindidzaleka kupempherera mtendere ndi madalitso a mtundu wanu, chifukwa pamenepo padzakhala madalitso anga ndi a banja langa. Ambuye, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale zanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa