Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 1:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Kulikonse anthu amapereka nsembe zofukiza ndi mphatso zangwiro m'dzina langa. Pajatu dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:11
65 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.


Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.


Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.


Ndipo adzaimbira njira za Yehova; pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.


Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.


Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi.


Monga dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi; m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.


Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.


kuti njira yanu idziwike padziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse.


Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.


Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.


Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.


Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.


Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.


Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi aakulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;


kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.


Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.


Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.


kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.


Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.


Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo.


chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;


Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.


Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.


kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa