Zekariya 12:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 “Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 “Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa. Onani mutuwo |