Ndili mwana wake wa Mulungu, ndikukumbukira kuti kale tinali titatayika, osadziwa komwe tikupita. Tsogolo lathu linkaoneka ngati nyanja yamoto, malo a zowawa zosatha, odzaza ndi kulira ndi kutaya mtima.
Koma Mulungu, m’chikondi chake chachikulu ndi chifundo, anatumiza Mwana wake kuti adzatipulumutse. Iye anatulutsa chigamulo chimene chinali pa ife. Yesu, Mpulumutsi wathu, anatsegula njira yoti tidzakhale naye kosatha.
Cholowa chathu ndi ichi, umboni wa ubwino ndi chikondi cha Mulungu, kutipulumutsa ku mphamvu ya uchimo. Monga momwe lemba la Aroma 3:23-24 limatiuza, “onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo akuyesedwa olungama mfulu mwa chisomo chake, mwa chiwombolocho chimene chili mwa Khristu Yesu.”
Tiyeyese kusunga nsembe yaikulu imeneyi, mwa kumvera mawu ake ndi kuchita chifuniro chake. Tiyeni tipitirizebe kuyenda m’njira yake, ndi kukhala moyo wotsatira mfundo zake. Mmenemo tidzapeza mtendere ndi machiritso, ndi kukonzekera nyumba yokongola imene Mulungu watikonzera.
Tiyeni tikhale moyo woyera, kuti tsiku lina tidzamuone Mulungu maso ndi maso, ndi kumulambira kosatha.
kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:
Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.
Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.
pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
ndipo afuula ndi mau aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.
angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,
kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.
Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine. Mwandipondetsa patalipatali, sanaterereke mapazi anga.
Pakuti Mulungu sanatiike ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,
Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.
Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo. Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.
koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.
Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha? Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe kukasupe wa madzi a moyo kwaulere. Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu, amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa.
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;