Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:47 - Buku Lopatulika

47 Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:47
35 Mawu Ofanana  

Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;


Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.


kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.


kuti Khristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.


Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa