1 Samueli 31 - Buku LopatulikaSaulo ndi ana ake atatu aphedwa ndi Afilisti pa Gilibowa ( 1Mbi. 10.1-12 ) 1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. 2 Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo. 3 Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo. 4 Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera. 5 Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye. 6 Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija. 7 Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo. 8 Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa. 9 Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu. 10 Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani. 11 Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo, 12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko. 13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi