Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 31:12 - Buku Lopatulika

12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 amuna ena olimba mtima adanyamuka, ndipo adayenda usiku wonse, nakachotsa mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake ku khoma la Beteseani. Atabwerera ku Yabesi adatentha mitemboyo kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 31:12
6 Mawu Ofanana  

anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.


Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.


udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.


Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.


Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa