Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 31:13 - Buku Lopatulika

13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli m'Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pambuyo pake adatenga mafupa ao naŵakwirira patsinde pa mtengo wa mbwemba ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 31:13
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.


Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.


Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.


Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake.


koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.


Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala mu Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa