Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 31:4 - Buku Lopatulika

4 Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke ndi kundipha.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 31:4
19 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;


Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?


Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.


Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;


Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mzinda, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa;


Ndipo machitidwe ena a Omuri anawachita, ndi mphamvu yake anaionetsa, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera.


Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana aakazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.


Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa