1 Samueli 31:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Aisraele amene anali tsidya lina la chigwa cha Yezireele, ndiponso amene anali tsidya lina la Yordani, ataona kuti anzao adathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake adafa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo. Onani mutuwo |