1 Samueli 31:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraelewo adathaŵa Afilisti, ndipo ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. Onani mutuwo |
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.