ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
Yohane 6:1 - Buku Lopatulika Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Yesu adaoloka nyanja ya Galileya (dzina lake lina ndi nyanja ya Tiberiasi.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), |
ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.
Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;
Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.
koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.
ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.