Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 9:10 - Buku Lopatulika

10 Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Apo anthu aja adamufunsa kuti, “Nanga maso ako apenya bwanji?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 9:10
11 Mawu Ofanana  

Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.


Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?


nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.


Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji?


Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya.


Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.


koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.


Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?


Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene.


Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa