Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 12:3 - Buku Lopatulika

3 ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Dzikolo lidaphatikizaponso chigwa cha Yordani, kuyambira kumwera kwa nyanja ya Galilea, kumapita cha ku Beteyesimoti, mzinda umene uli pafupi pa Nyanja Yakufa, mpaka kumwera ndithu, patsinde pa phiri la Pisiga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 12:3
15 Mawu Ofanana  

Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).


ndipo anaononga mizindayo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'mizindamo, ndi zimene zimera panthaka.


Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.


chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumizinda, kumizinda yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu,


atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.


ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa.


ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum'mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga.


ndi kwa mafumu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kuchigwa kumwera kwa Kineroti, ndi kuchidikha, ndi ku mitunda ya Dori kumadzulo;


ndi Betepeori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beteyesimoti;


Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;


Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa