Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pambuyo pake Yesu adachoka kumeneko, nayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya. Kenaka adakwera m'phiri nakakhala pansi kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:29
12 Mawu Ofanana  

Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya wa amitundu.


Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.


Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake;


Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.


Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;


ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa