Numeri 8:17 - Buku Lopatulika Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. |
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.
Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.
(monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)
kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?
Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;
Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.