Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:16 - Buku Lopatulika

16 Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndithudi, iwoŵa aperekedwa kwathunthu kwa Ine pakati pa Aisraele. Ndaŵatenga kuti akhale anga m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa, ana achisamba onse a Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:16
6 Mawu Ofanana  

Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.


Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.


Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.


Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.


Sendera nalo kuno fuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.


Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa