Numeri 8:17 - Buku Lopatulika17 Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. Onani mutuwo |