Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 pakuti ana onse aamuna oyamba kubadwa ndi anga. Pa tsiku lija lomwe ndidapha ana onse aamuna oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, ndidadzipatulira ana onse oyamba kubadwa a m'dziko la Israele, ana a anthu ndi a nyama omwe. Onsewo ndi anga, Ine ndine Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:13
16 Mawu Ofanana  

ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;


kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.


ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.


Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.


Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.


Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.


Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.


Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.


Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.


Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.


Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele.


pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.


(monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)


ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa mu Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa