Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake amuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Chihema chamsonkhanocho ndidzachisandutsa kuti chikhale chopatulika, pamodzi ndi guwa lomwe. Ndipo Aroni ndidzampatula pamodzi ndi ana ake aamuna, kuti akhale ansembe anga onditumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:44
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao.


Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.


ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.


kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa