Eksodo 29:43 - Buku Lopatulika43 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201443 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa43 Kumeneko ndiko ndizidzakumana ndi Aisraele, ndipo malo amenewo azidzakhala oyeretsedwa chifukwa cha ulemerero wanga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero43 Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga. Onani mutuwo |
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;