Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Numeri 6:24 - Buku Lopatulika Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga; |
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
chifukwa chake tsono chikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu chikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munachinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.
Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.
Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.
Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;
Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pamalo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye.
Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.
Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,
Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.