Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Numeri 4:5 - Buku Lopatulika akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake amuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene anthu akusamuka pamodzi ndi mahema ao, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe m'chihema chamsonkhano, amasule nsalu yochinga, ndipo aphimbire Bokosi laumboni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni. |
Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.
Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.
Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.
Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse.
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.
Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri:
Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.
Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;
Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.
Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.