Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 36:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Pambuyo pake adapanga nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo adapetapo zithunzi za akerubi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 36:35
8 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.


Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.


Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide.


Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.


nalowa nalo likasa mu chihema, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;


pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa