Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake amuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene anthu akusamuka pamodzi ndi mahema ao, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe m'chihema chamsonkhano, amasule nsalu yochinga, ndipo aphimbire Bokosi laumboni.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:5
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.


sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”


Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi.


Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi.


Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani.


Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.


Iye adzachotsa kulira kumene kwaphimba anthu ngati nsalu. Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.


Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.


Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu.


“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.


“Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri.


Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo.


Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.


Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli.


Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.


Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri.


Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa