Numeri 4:15 - Buku Lopatulika15 Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Atatha Aroni ndi ana ake amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati adze m'chihema chokomanako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Tsono Aroni ndi ana ake, atamaliza kuphimba malo opatulika pamodzi ndi zipangizo zake zonse, pamene anthu akusamuka, ana a Kohati ndiwo abwere kudzanyamula zimenezi, koma asakhudze zinthu zopatulika, kuti angafe. Zimenezi ndizo zinthu za m'chihema chamsonkhano zimene ana a Kohati azinyamula. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 “Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano. Onani mutuwo |