Numeri 4:14 - Buku Lopatulika14 Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake. Onani mutuwo |