Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:14
7 Mawu Ofanana  

Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu: guwa lansembe lagolide; matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;


“Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229.


Upange ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika yochotsera phulusa, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto.


“Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake.


“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.


Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa