Numeri 4:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa Kachisi opatulika, ndi zipangizo zake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 “Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 “Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.” Onani mutuwo |