Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa Kachisi opatulika, ndi zipangizo zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:16
20 Mawu Ofanana  

mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira;


Ndipo Yehova anati kwa Mose,


ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.”


Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa.


Yehova anawuza Mose kuti,


“Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse.


“Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo.


Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika.


Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti,


“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,


Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake.


Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu.


Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.


Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.


Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.


Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.


Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa