Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 16:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni mbale wako kuti asamaloŵa nthaŵi iliyonse ku malo opatulika kwambiri, kuseri kwa nsalu yochinga, pamaso pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi lachipangano, kuti angafe, chifukwa Ine ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 16:2
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.


Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.


ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.


Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.


Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.


Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.


Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.


Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.


koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.


akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,


Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;


chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;


kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;


Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;


ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.


Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa mu Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa