Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
Numeri 19:12 - Buku Lopatulika iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asambe ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri kuti ayere, ndipo adzamuyeretsadi. Koma akapanda kusamba pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti ayere, sadzayera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. |
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lake, namutche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.
Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.
Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.