Numeri 19:13 - Buku Lopatulika13 Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa Kachisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Munthu aliyense wokhudza munthu wakufa, ndipo sadziyeretsa, munthu ameneyo akuipitsa Chihema cha Chauta, choncho adzachotsedwa m'dziko la Aisraele. Akhale woipitsidwa chifukwa sadawazidwe madzi aja oyeretsera pa zachipembedzo, ndi woipitsidwabe ameneyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo. Onani mutuwo |