Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 19:14 - Buku Lopatulika

14 Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Pamene munthu afera m'hema, lamulo lake nali: munthu aliyense amene aloŵa m'hemamo, ndipo aliyense amene ali m'hema, akhale woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:14
13 Mawu Ofanana  

Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.


Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.


Ichi ndi chilamulo cha nthenda iliyonse yakhate, ndi yamfundu;


Ichi ndi chilamulo cha wakukha, ndi cha iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;


Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.


Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.


Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.


Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.


Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;


Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.


Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.


Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa