Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 19:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Asambe ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri kuti ayere, ndipo adzamuyeretsadi. Koma akapanda kusamba pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti ayere, sadzayera.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:12
12 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera, munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala


ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona.


Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.”


Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse.


Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa; pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.


Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.


Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto.


“Inu nonse amene mwaphapo wina wake, kapena kukhudza aliyense amene anaphedwa mukhale kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachitatu mudziyeretse nokha pamodzi ndi akapolo anu.


Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro.


Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa